Copyright, Voice Of God Recordings - SLIDEBLAST.COM

Ndipo. Mawu a Ambuye amadza kwa mneneri. Ndipo kodi Iwo amachita motani izo? Iwo amawonetsera Mawu a Mulungu. Kuwonetsera kwa Mulungu, kumene ...
107KB Größe 2 Downloads 124 vistas
MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

1

Mulungu Ndi Wodzitanthauzira Yekha ` Atate athu Akumwamba, Mawu ochokera kwa Inu angatanthauze mochuluka kuposa zonse zimene anthu pa nthawi iliyonse akanakhoza kuchita kapena kunena, chifukwa anthu akuyembekeza kuti akuwoneni Inu. Ndipo ife tikukuthokozani Inu chifukwa pali iwo amene ali pansi pa kuyembekezera, iwo akuyang’anira kuti chinachake chichitike. Ndipo pamene anthu ali ndi ludzu la chinachake, chakuya chikuyitanira ku Chakuya, payenera pakhale Chakuya kuti chiyankhire ku kukuitana uko. Ndipo ndicho chifukwa ife tiri pano usikuuno, chifukwa chinali pa mtima wa azitumiki awa, ndi anthu, kuti atiyitanire ife palimodzi kuti tikupempheni Inu chifundo ndi madalitso, tikukhulupirira kuti Inu muchiritsa odwala ndi kupulumutsa otayika, ndipo muwonetsera Mawu Anu. 2 Ndipo ife tikupemphera, Atate Akumwamba, kuti Inu mupereke izi kwa ife pamene ife tikuyembekezera modzichepetsa pa Inu, usiku ndi usiku. Mulole pakhale kotero_kutsanulira kwa Mzimu Woyera, ndipo mulole munthu aliyense akhale wakhungu kwa china chirichonse pozungulira iwo kupatula Mulungu. Mulole pakhale kulira kwakukulu kotero kupite uko pakati pa anthu, aludzu kwa Mulungu, mpaka padzabwere chitsitsimutso ku dziko lonse kuno ndipo mpingo uliwonse ukhale wolongezedwa modzaza ndi anthu, ochimwa akulirira kwa Mulungu kuti apeze chifundo, ndi_ndipo Mzimu Woyera kuchiritsa odwala, kuwapangitsa olumala kuyenda, ndi kuwukitsa akufa, ndi kupereka zinthu izi zimene zinalonjezedwa mu Mawu Anu. 3 Bwerani, Ambuye Yesu, ndi kudzakwaniritsa lonjezo Lanu. Bwerani kwa ife usikuuno. Ife tikukhulupirira kuti Inu muli yemweyo dzulo, lero, ndi kwa nthawizonse, kuti malonjezo Anu sangakhoze kulephera. Zonse mmwamba ndi dziko lapansi zidzalephera koma Mawu Anu sadzalephera ayi. Mulole kumvetsa kwathu kukhale kotseguka. Mulole Mzimu Woyera ubwere ndi kudzayala nthaka yosalimidwa. Mulole kumvetsa kwathu kukhale kotseguka kwa Mzimu ndi mphamvu ya Mulungu usikuuno, kuti Iye akhoze kumawonetsera Mawu Ake olonjezedwa kupyolera mwa ife. Pakuti ife tikupempha izi mu Dzina la Yesu. Ameni. 4 Tsopano, usikuuno, inu amene mukuyembekezera mutu, tiyeni titembenuzire mu Baibulo ku Bukhu la ll Petro, ndipo tiyambire ndi ndime ya 15, basi mwanjira ya kuyankhula pa Lemba kwa mphindi zingapo.

2

MAWU OLANKHULIDWA

Kuwonjezera apo ndiyesetsa kuti inu mudzakhale okhoza ine nditamwalira kukhala mukuzikumbukira zinthu izi nthawizonse. Pakuti ife sitinatsatire ndale zochenjera, nthano, pamene ife tinakudziwitsani inu mphamvu ndi kudza kwa Ambuye Yesu Khristu, koma tinali mboni zapamaso za ukulu wake. 5 Ine ndikuzikonda izo, “mboni zapamaso.” Osati nthano ina. Ndife mboni za chimene ife tikuchikamba. Pakuti iye analandira kuchokera kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, ndipo panadza liwu lotero kwa iye lochokera ku ulemerero waukuru, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, mwa yemwe Ine ndiri wokondweramo bwino. Ndipo liwu ili limene linabwera kuchokera kumwamba ife tinalimva, pamene ife tinali ndi iye mu phiri lopatulika. Ife tiri nawonso mau otsimikizika ochuluka achinenero; amene inu mukhoza kuchita nawo bwino kuti inu mukhale osamalira, monga ngati kwa nyali younikira mu^malo a mdima, mpaka tsiku litacha, ndi nyenyezi ya tsiku itatulukira mu mitima yanu. Podziwa ichi poyamba, kuti palibe uneneri wa lemba uli ndi kutanthauzira kwa mseri kulikonse. Pakuti uneneri sunadze mu nthawi zakale mwa chifuniro cha munthu: koma anthu oyera a Mulungu ankayankhula pamene iwo anali kusunthidwa ndi Mzimu Woyera. 6 Ambuye atawonjezera madalitso Awo ku kuwerenga kwa Mawu Ake. Tsopano, ine ndikuti nditenge izi mwa phunziro: Mulungu Ndi Wodzitanthauzira Yekha. 7 Ife tikukhala mu tsiku la chisokonezo. Ife tikukhala mu tsiku pamene amuna ndi akazi sakudziwa nkomwe choti nkuchita. Chirichonse, chiri_chikuwoneka kuti chiri mu chisokonezeko. Chirichonse, zikuwoneka kuti pali njira zambiri zosiyana zoti uyang’aneko. Ndiye Satana, amene akuchita izo. 8 Tsopano, Mulungu sangakhoze kuwaweruza anthu mwachirungamo, molungama, kupatula ngati patakhala muyezo wina umene Iye ayenera kuti aziwaweruzira nawo. Ndipo Baibulo limanena kuti Iye adzaweruza anthu onse ndi Yesu Khristu, ndipo Yesu Khristu ndiye Mawu. Mu Yohane Woyera, mutu wa 1. Ilo limati: Pa chiyambi kunali Mawu, ndipo Mawu anali ndi Mulungu, ndipo Mawu anali Mulungu.

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

3

Ndipo Mawu anapangidwa thupi, ndipo anadzakhala pakati pathu,^ 9 Tsopano, zonse zimene ife tiri lero ndi chiwonetsero cha zikhumbo Zake. Mwa Mulungu^Choyamba Iye sanali ngakhale Mulungu, Mulungu, ife tikhoza kungomutcha Iye “Iye Wamuyayayo.” Iye sanali Mulungu, chifukwa mawu (mawu Achingelezi) Mulungu amatanthauza “chinthu chopembedzedwa” ndipo panalibe kanthu koti kazimupembedza Iye. Chotero Iye anali Iye Wamuyayayo, Kasupe we_weniweni wa luntha lonse. Ndipo mu Kasupe uyu wa luntha lonse kunali kopanda atomu, molekyulu, kapena kena, kuwala panalibe, nyenyezi, mwezi, popanda kalikonse. Mulungu, chimene ife timachidziwa ngati Mulungu, Mzimu waukulu umene unali Wamuyaya (sunayambe konse, sunathe konse), Iye analipo. Ndipo mwa Iye munali zikhumbo: zikhumbo zinali kuti akhale Mulungu, kenako zikhumbo Zake kuti akhale Atate, zikhumbo kuti akhale Mwana, zikhumbo kuti akhale Mpulumutsi, zikhumbo kuti akhale Mchiritsi. Zikhumbo zonse izi zinali mwa Iye. Ndipo tsopano Iye^Zinthu izi zimene zafutukulidwa kuyambira apo ziri zikhumbo Zake chabe kukhala zikuwonetseredwa. 10 Chimene ine ndikutanthauza, zikhumbo zinali “maganizo” Ake. Ndipo m_mawu ndi “ganizo lofotokozedwa.” Ndiyeno izo zinali mu kuganiza Kwake. Ndipo pamene Iye anati, “Apo pakhale,” ndipo apo panali. “Apo pakhale,” ndipo apo panali. 11 Ndipo tsopano, kumbukirani, Akhristu inu munali maganizo Ake pasanakhale dziko. Ndipo inu ndinu chiwonetsero cha kuganiza Kwake. Pasanakhale ngakhale dziko, inu munali mwa Khristu, (ameni) mwa Mulungu pa chiyambi. Izo zikukupangani inu, ndiye, inu mukuona, omvera Ake. Ndipo chinthu chonsecho ndi Mulungu, Mwiniwake, akudzipangitsa Mwiniwake chogwirika kotero Iye akanakhoza kumagwiridwa, kuwonedwa, ndi_ndi zina zotero. Ndipo ndicho chimene Mulungu ali, chinthu chonsecho. 12 Ndiye anthu amati, “Kutanthauzira^” Ine ndinali kuyankhula kuno osati kale litali mu msonkhano, mwamuna ananena kwa ine, iye anati, “M’bale Branham, inu muli ndi kutanthauzira kolakwika. Inu simukutanthauzira Izo molondola.” 13 Tsopano, ife timamva^Iwo amapita ku Methodisti, ndipo iwo amati “Achibaptisti samatanthauzira molondola.” Achibaptisti amati, “Achipentekoste satero.” Achipentekoste amanena kuti “A_Aumodzi satero. Aumodzi amati, “Assemblies satero.” Ndipo aliyense amati enawo satero. 14 Mulungu ndi Wodzitanthauzira Yekha! Iye samasowa aliyense kuti azimutanthauzira Iye. Iye amachita

4

MAWU OLANKHULIDWA

kutanthauzira Kwake Kwake. Munthu ndi ndani kuti angakhoze kumutanthauzira Mulungu? Mulungu ndi Wodzitanthauzira Yekha. 15 Tsopano, Petro akuyankhula apa, ife tikupeza kuti pa chiyambi pamene Mulungu anati, “Pakhale kuwala,” ndipo panali kuwala, ndiko kutanthauzira kwa izo. Pamene Mulungu ananena chirichonse ndipo icho chinawonetseredwa, ndiye ndiko kutanthauzira kwa Mulungu kuti Mawu Ake ndi olondola. Mwaona? Pamene Iye anati, “Pakhale kuwala,” izo zinali mu kuganiza Kwake poyamba pasanakhale chinthu choterocho monga kuwala. Pamene Iye anati, “Pakhale kuwala,” kuwala kunatulukira mu mlengalenga, ndiko kutanthauzira. Palibe munthu ayenera kutanthauzira izo, pakuti Mulungu ananena chomwecho ndipo apo izo zinali. Pamene Mulungu ayankhula ndipo izo nkuwonetseredwa, ndiko kutanthauzira kwa Mawu Ake. Nchifukwa chiyani kuti athu samawona izo? Nchifukwa chiani anthu sali kuziwona izo? 16 Pamene Mulungu akapanga lonjezo ndipo Mulungu nkuti^Pa_pachiyambi, mu Genesis, Iye anawagawa Mawu Ake kwa m’badwo uliwonse pamene Iwo amabwera mmusi kuchokera kuchiyambi mpaka kumapeto. Ndipo, mpaka kupyola mibadwo iyi, dziko la mpingo liri nazo zinthu zonse izi atazisokoneza ndi miyambo, ndi zina zotero, ndipo Mulungu nthawizonse amatumiza powonekera, monse kupyola mu Chipangano Chakale ndi Chatsopano, aneneri! Ndipo Mawu a Ambuye amadza kwa mneneri. Ndipo kodi Iwo amachita motani izo? Iwo amawonetsera Mawu a Mulungu. Kuwonetsera kwa Mulungu, kumene kumatiuza ngati ziri zolondola kapena zolakwika. Palibe wina ayenera kuwatanthauzira Iwo, Mawu amadzitanthauzira Okha. Mulungu analonjeza izo ndipo apo izo zimachitika! 17 Zimachita ubwino wanji kuti unene china chirichonse za Iwo? Ndi ndani munthu wochimwitsitsa yemwe angayesere kunena (pamene Mulungu anapanga lonjezo ndipo Mulungu nkuzipanga izo) nkuti kutanthauzira kumeneko ndi kolakwika? Uyo ndi Mulungu Mwiniwake akupanga kutanthauzira Kwake Kwake, kutanthauzira. Iye samasowa wina aliyense kuti amutanthauzire Iye, Iye amatanthauzira Yekha pa kuwonetsera chimene Iye analonjeza kuti Iye akanati adzachite. 18 O, ngati mpingo ukanakhoza kungoziwona izo ndi kuwona malonjezo amene anaikidwa kwa m’badwo uliwonse! Mibadwo ina yonse, Mulungu waitumiza powonekera (ngakhale monse kupyola mu mibadwo isanu ndi iwiri ya mpingo) ndipo wawonetsera chirichonse chimene Iye analonjeza kuti achita. Chirichonse, palibe chinthu chimodzi chimene chasiyidwa chosachitidwa. Ndendende! Chimene Iye anati Iye akanati achite, chimenecho Iye anachichita.

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

5

19 Chifukwa pamene Mulungu ananena, mmbuyo umo mu Yesaya, Iye anati, “Namwali adzaima,” ndipo iye anatero. Tsopano, ndani_ndani angakhoze kutanthauzira izo? Mulungu anachita kutanthauzirako. Iye anati, “Namwali adzaima,” ndipo iye anaima. Tsopano, ndinu ndani^inu simungakhoze^Palibe chimene chinganenedwe pa izo, chifukwa Mulungu anati iye akanadzatero ndipo iye anachita izo. Koma mpingo unali wakhungu kwambiri apo kuti uziwone izo. Mwaona, iwo anali ndi lingaliro lawo lawo la izo. Izo zinali kwambiri_zosiyana kwambiri ndi zimene iwo anali kuziyembekezera. 20 Petro apa anali kulozera mmbuyo, iye anati, “Mulungu anamuwonetsera Khristu mwa Mawu Ake, Iye anati, ‘Uyu ndiye Mwana Wanga wokondedwa.’ ” Okhulupirira awa anali ataima apo. Ndipo Khristu anali kuwonetseredwa kwa Mulungu. Iye nthawizonse ankamuwonetsera Khristu mwa Mawu Ake, chifukwa Khristu ndiye Mawu. Iye amawonetsera nthawizonse. 21 Pamene Iye anatero^Mu masiku a Nowa, Khristu anali mwa Nowa. Kodi inu mukukhulupirira izo? Nowa anati, “Iyo ikanati ivumbe. Kudzakhala kuli mvula, dziko lapansi lidzawonongedwa.” Iyo inavumba. Izo sizinasowe kutanthauzira kulikonse. Iyo ikanati ivumbe chifukwa Mulungu, mwa Nowa, anati, “Iyo idzavumba.” Iye anali mneneri, ndipo umboni unali kuti zimene iye ananena zinafika pochitika. Chotero iwo sasowa kuti azitanthauzira izo. 22 Ena a iwo akhoza, pamenepo, kuti, “Munthu uyu sakudziwa chimene iye akuchinena.” 23 Koma Mulungu nthawizonse anali atalonjeza, “Ngati pakhala pali mmodzi pakati panu yemwe ali wauzimu, kapena mneneri, ndipo zomwe iye anena zikafika pochitika, ndiye mverani izo.” Ndiko kulondola, chifukwa ndi zoona. Izo ziyenera kukhala molingana ndi Mawu. Ndipo Nowa anali molingana ndi Mawu. Pamene iye analonjeza kuti iyo ikanati ivumbe, ndipo iyo inavumba. Izo sizinasowe kutanthauzira kulikonse kwa izo, chifukwa iyo inachita zomwezo basi. 24 Yesaya anati, “Namwali adzaima,” ndipo iye anatero. Tsopano, izo zinali zosazolowereka kwambiri. Pakuti, onani, izo zinali zaka mazana ambiri mtsogolo namwali uyu asanaime. 25 Izo zinali zosazolowereka kwambiri mpaka munthu wabwino dzina lake Yosefe, mwamuna wake, “pokhala munthu wolungama ndipo sanali kulolera kuti amupange iye chitsanzo cha pagulu^” Munthu wabwino uyo mu masiku amenewo, momwe izo zikanakhalira kuti zinali kwa Yosefe pamene iye anali atatomerana, atapalana ubwenzi ndi Maria.

6

MAWU OLANKHULIDWA

26 Iye anapalidwa ubwenzi. Mu tsiku ilo, kuti aswe izo, zinali basi zofanana ngati kuchita chigololo. Ndipo, ndithudi, kwa Yosefe, izo zinkawoneka ngati kuti Maria anali kuyesa kumugwiritsa iye ntchito ngati chodziphererera, kapena kumupanga iye kuti akhale chishango kwa cholakwa chake, chifukwa apa iye anapezeka ali woyembekezera, asanakwatiwe, wotomeredwa kokha. Kuchenjera konga uko, akanati agendedwe mpaka kufa; izo zikanayenera kutero, mwa lamulo. 27 Ndipo Yosefe, mwamuna wake, anali munthu wolungama, munthu wolungama kwambiri. Iye ankakhulupirira Mulungu. Ndipo pamene anayang’ana pa iye ndi maso okondeka awo, aakulu ofewa, ndi kuti, “Yosefe, Gabrieli Mngelowamkulu anadzandichezera ine ndipo wandiuza ine kuti ine ndiima, mosamudziwa mwamuna aliyense.” 28 Tsopano, ngati Yosefe akanangoti ayang’ane mmbuyo mu Lemba, mneneri anati iye akanadzachita izo! Uyo anali Mulungu yekha akutanthauzira Mawu Ake Omwe! Mwaona? Koma izo zinali zosazolowereka kwambiri. 29 Ndilo liri vuto mu m’badwo uliwonse. Mawu a Mulungu ndi achilendo kwa anthu; Izo nzosazolowereka kwambiri. Mulungu nthawizonse amachita zosazolowereka. Ndi zosazolowereka kulikonse kumene Mulungu ali. Izo zimatsutsana ndi kachitidwe ka mdziko, chifukwa kuti iwo ali nazo zinthu mwanjira imene iwo akuganiza kuti izo ziyenera kukhalira. Koma Mulungu amabwera umo ndipo amachita zosazolowereka. 30 “Namwali uyu akanaima chotani?” Iye anali woonamtima, iye anafunsa Mulungu pa izo. 31 Ndiyeno Mulungu anayankhula kwa iye mu loto, ndipo anati, “Yosefe, iwe mwana wa Davide, usawope kudzitengera kwa iwe Maria mkazi wako, pakuti icho chimene chiri choyembekezeredwa mwa iye ndi cha Mzimu Woyera. Mulungu wamufungatira iye. Ichi ndicho chomwe chachita izo.” 32 Kodi inu munayamba mwazindikirapo momwe Mulungu anachitira ndi Yosefe apo? Mwa njira yachiwiri, mwa njira ya loto. Tsopano, ife tikudziwa pali maloto, ife timakhulupirira mu maloto. Ine ndimakhulupirira mu maloto. Ndakhala^Mulungu nthawizonse wachita ndi anthu mu maloto. Koma maloto ndi chachiwiri, mukuona, izo zikhoza kukhala zolondola kapena zolakwika kupatula izo zitatanthauziridwa. Koma iye sanasowe kutanthauzira kulikonse. Izo anali Mulungu Iyemwini akuyankhula molunjika kwa Yosefe, chifukwa panalibe mneneri mu dziko mu masiku amenewo kuti atanthauzire. Uko anali asanakhale ndi mneneri kwa zaka mazana anai. Chotero chopambana

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

7

chotsatira, chimene Mulungu ankasamalira chochitika_nkhani ya mwana Wake Yemwe, chinali kuti ayankhule kwa Yosefe kupyolera mu loto ndipo popanda kutanthauzira. Iye anati, “Mkaziyo akulondola. Chinthu Choyera icho chimene chiri choyembekezeredwa mwa iye ndi Mwana wa Mulungu.” Sizinasowe kutanthauzira kulikonse. 33 Mulungu amachita kutanthauzira Kwake Kwake kwa mitima yoona, yodzipereka, amuna ndi akazi amene amayang’ana pa_chinthu chimene chiri chachinsinsi, ngati muli owonamtima ndi odzipereka ndipo mukati mukhulupirire, Mulungu ali nayo njira yotanthauzirira izo kwa inu. Choyamba, mupeze ngati ilo liri lonjezo. Ngati Yosefe akanangoti abwerere nachoka ku miyambo ndi kubwerera ku Baibulo, ndi kukazifufuza, Yesaya anati iye akanati adzachite izo. 34 Ndipo zinthu zimene zinanenedwazo, ndi kubadwa Kwake, ndi zonse za izo zinanenedwa ndi Malemba, “ndi aneneri oyera,” monga Petro ananena. Ndipo palibe munthu ali nawo ufulu kuti aziyika kutanthauzira kwamseri kwa izo. Ndizo ndendende basi zimene Mulungu anati zikanadzachitika. Iye anali chiwonetsero cha Mawu a Mulungu olonjezedwera kwa tsiku limenelo. Mulungu ananena izo, chotero apo izo zinali. Izo zinakhazikitsa icho. 35 Yesu anati^Pamene Iye anali pa dziko lapansi, pamene iwo sankakhoza kuumvetsa utumiki Wake, iwo unali wawukulu kwambiri, wododometsa kwambiri, (iwo sakanakhoza), kudodometsa, kani. Iwo sankakhoza kumumvetsa Iye. Iye anati, “Fufuzani Malemba!” (Ine ndikuyembekeza ine sindikukugonthetsani inu kunja uko, kulindima mu icho.) “Fufuzani Malemba, pakuti mwa Iwo inu mumaganiza kuti inu muli nawo Moyo Wamuyaya, ndipo ndi Iwo amene akuchitira umboni za Ine.” Mwaona? “Iwo ndi Omwe akukuuzani inu Yemwe Ine ndiri.” 36 Mukuona, Mulungu anagawa Mawu. Tsiku limenelo linkayenera kukhala la kuwonetseredwa kwa Mulungu, Mulungu (Emanuele) nafe, “Dzina Lake adzatchedwa Wodabwitsa, Wauphungu, Kalonga wa Mtendere, Mulungu Wamphamvu, Atate Wosatha. Ndipo Dzina Lake adzatchedwa Emanuele, ‘Mulungu nafe.’” Mulungu anali mwa Davide. Mulungu anali mwa Mose. Mulungu! Ameneyo ndi Mulungu njira yonse kudutsa, akudziwonetsera Mwiniwake kwa m’badwo umenewo. Koma m’badwo uwu, “Namwali adzatenga pakati ndipo iye adzabala Mwana, ndipo Iye adzakhala Mulungu nafe.” 37 Ndicho chifukwa chimene iwo anamupachikira Iye, akudzipanga Yekha Mulungu, ndiponso chifukwa cha kuswa Sabata. Iye anali_Iye anali Mulungu wa pa Sabata, ndipo Iye

8

MAWU OLANKHULIDWA

anali Mulungu. Ndipo Iye sanali munthu wamba chabe kapena mneneri wamba (komabe Iye anali Munthu wamba ndi Mneneri), koma Iye anali Mulungu-Mneneri. Ndipo Iye anali kukwaniritsa kwa Mawu, ndendende chimene Mulungu anati Iye akanadzachita. Anati, “Ndani mmodzi wa inu angakhoze kunditsutsa Ine za tchimo? Fufuzani Malemba! Mwa iwo inu mukuganiza kuti inu muli nawo Moyo Wamuyaya, ndipo iwo ndi amene akuchitira umboni za Ine.” Koma miyambo yawo, iwo anali akukhala mu kunyezimira kwa m’badwo wina. 38 Monga ine ndinali kulalikira masabata angapo apitawo, “Kukhala mu kunyezimira.” Kunyezimira ndi “ngatimadzi,” dzuwa likudzinyezimiritsa lokha, ndipo iko ndi kwabodza. Ndipo kunyezimira kulikonse kwa m’badwo wina ndi kuwalitsira kwa bodza. Anthu nthawizonse akumayenda mu chinachake chimene chinachitika zaka zakale. Achilutera akuyenda mu kunyezimira kwa Chilutera. Kuwala kwa dzuwa kwa Lutera kunali kwabwino mu tsiku lake; kwa Wesile kunali kwabwino mu tsiku lake; kwa Chipentekoste kunali kwabwino mu tsiku lake. Ife tikupita chokwera makwerero, ife tikukhala mu m’badwo wina! Ife tikupitirira, kupitirira, ife sitingamapitirize kuyang’ana mmbuyo. 39 Pamene ife tifika podzikhazikitsa tokha pansi mu zinthu, ife timaganiza kuti ife tazipanga izo zonse, ife timazikutira ndi miyambo yathu; ndipo izo zonse zinali zabwino kwa tsiku ilo, koma ife tikusuntha mopitirira! Fufuzani Malemba ndi kuwona chimene chalonjezedwera kwa lero, ndiye ife tidziwa pamene ife tiri, ndiye ife tikhoza kudziwa pamene ife taima. 40 Lutera; iwe ukhoza kuyang’ana mu Lemba ndi kuwona mwa iwo_mu m’badwo wa Sarde uwo, iwe ukhoza kuwona ndendende zimene zinalonjezedwa. Kuyang’ana mtundu wa womkwera amene anapitapo, kuyang’ana chimene chinapita kuti chikakomane ndi Iye, ndendende, “kuchenjera kwa munthu,” kukonzanso. Kumuwona Wesile, ndi ena otero. Pamene izo zimabwera mpaka mmusi kumka ku m’badwo wa Chipentekoste, ndi mmusi kupyola mu m’badwo umenewo, kuwona momwe izo zayendera. Kuyang’ana pa Malemba ndi kuwona pamene ife tiri. Ndicho chifukwa Yesu anati, “Fufuzani Malemba!” 41 Onani pamene ife tiri! Ine ndikukhulupirira ife tiri pa Kudza kwa Mwana wa Mulungu pakali pano. Ine ndikukhulupirira ife tiri pa m’badwo wa_ora lomwe loti Iye akhoza kuwonekera pa nthawi iliyonse. Ine ndikukhulupirira Malemba akunenetsa izo, kuti ife tiri mu maora otsiriza a mbiriyakale ya dziko lino. Ine ndikukhoza kuwona zinthu pamene izo zikusongoka. Kuwona Khonsolo ya Zipembedzo iyi ikutsogolera mipingo yonse kukalowa mu iyo, kukalowa mu Chilemba cha chirombo. Ndi ndikuwona Ufumu wa Chiroma

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

9

ndi chimene iwo ukuchita, ndi ena onse a iwo. Kuwawona iwo akubwera palimodzi, kutsekera panja Kuwala, kutsekera panja Uthenga. Aliyense ayenera kukhala wa mu iyo ndi kumayenda mu kuwala kwake kapena iwe suyenda konse. Mwaona, ife tiri pa nthawi yotsiriza. Palibe kanthu katsalira kwa ife koma kuti tigwiritse kwa Mulungu ndi kukhulupirira Mawu Ake. Mawu ali nthawizonse olondola. 42 Mu m’badwo wa mpingo wa Laodikaya, uwo unali m’badwo wa mpingo wokha, wa yonseyo, umene Khristu anaikidwa kunja kwa mpingo. Iye anali kunjako, akugogoda. Nchiani chinachitika? Khonsolo ya Zipembedzo iyi ndi yomwe iti idzamuike Iye kunja. Baibulo linati Iye anali woti akhale ali kunja, ndipo Iye ali. Iwo ukutsekera panja chiani? Mawu. Ndipo Iye ndiye Mawu, Iye nthawizonse wakhala ali Mawu, ndipo Iye akadali Mawu panobe usikuuno! Iye ali Mawu. 43 Baibulo linati, “Mawu ndi akuthwa, amphamvu kwambiri kuposa lupanga lakuthwa konsekonse,” Ahebri, mutu wa 4, “ozindikira malingaliro ndi zolinga za mtima.” Mawu anali! Iwo bwezi atazindikira Yemwe Iye anali pamene Yesu ankanena izo mu tsiku limenelo. 44 Penyani chimene Iye anachita. Tsiku lina Iye anali ataima pamenepo, pachiyambi penipeni pa utumiki Wake. Panali mwamuna anabwera kwa Iye, dzina lake Simoni, Simoni Petro. Ndipo pamene Petro anayang’ana pa Iye ndi_ndipo atamuwona Iye, Yesu ananena ndi iye, “Dzina lako ndiwe Simoni ndipo ndiwe mwana wa a Yonasi.” (Iye bwezi atadziwa kuti Mose anati, “Ambuye Mulungu wanu adzawutsa Mneneri wonga ine, ndipo Iye inu muyenera kumumvera.”) Ndipo apa panali Munthu yemwe anali asanayambe wamuwonapo iye mu moyo wake, anati, “Dzina lako ndiwe Simoni ndipo ndiwe mwana wa a Yonasi.” chifukwa, iye akanadziwa pomwepo kuti uyo sangakhoze kukhala winanso^Iwo sanakhale naye mneneri kwa mazana a zaka, ndipo apa panali Munthu akumuuza iye yemwe iye anali. Palibe zodabwitsa iye anakhoza kuzilandira izo! 45 Filipo, pa nthawi iyo, anapita ndi_ndipo anakamupeza Nataniele ali pansi pa mtengo, ndipo anamubweretsanso iye kwa Yesu. Yesu anati, “Taonani M’israeli mwa yemwe mulibe chinyengo.” Iye anati, “Rabbi, ndi liti pomwe Inu munandidziwa ine?” 46 Iye anati, “Filipo asanakuitane iwe, pamene iwe unali pansi pa mtengo, Ine ndinakuwona iwe.” 47 Iye anati, “Rabbi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu! Ndinu Mfumu ya Israeli.” Iye anadziwa kuti uyo anali! Chiani? Izo sizinasowe kutanthauzira kulikonse, Yehova ananena izo!

10

MAWU OLANKHULIDWA

48 Apo panaima iwo amene sanali kuzikhulupirira izo. Iwo anati, “Munthu uyu ndi Belezebule. Iye ali_Iye ali nawo mtundu wina wa tsenga lomwe Iye akulikoka. Iye_Iye ndi wambwebwe, kapena chinachake.” 49 Yesu anayang’ana pa iwo, ndipo anati, “Bwanji, inu mukayankhula izo momutsutsa Mwana wa munthu, izo zikhululukidwa kwa inu. Koma pamene Mzimu Woyera udzadza kudzachita chinthu chomwecho, nkuyankhula moutsutsa Iwo, izo sizidzakhululukidwa konse kwa inu, mu dziko lino kapena dziko likudza.” Iye anali kunenera za tsiku lathuli, tsiku limene ife tiyenera kuwona. Pakuti Iye ali yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. Kumbukirani, anali Yesu Khristu yemwe anali mwa Mose. 50 Anali Yesu Khristu yemwe anali mwa Davide. Pamene Davide, mwana wa^Davide anapita pamwamba pa phiri, mfumu yokanidwa, ndipo analirira pa Yerusalemu, izo sizinali kanthu kena koma Khristu mwa iye. Pakuti pafupi zaka eyiti handiredi mtsogolomo, Mwana wa Davide anadzakhala pamwamba pa Phiri la Azitona ndipo anayang’ana mmusi pa Yerusalemu ndipo analira, ndipo anati, “Yerusalemu, Yerusalemu, ndi mowirikiza bwanji ndikanati Ine ndikufungatire iwe monga nkhuku ingachitire anapiye ake, koma iwe sukufuna ayi!” 51 Pamene Yosefe anali mu ndende, uyo anali Yesu. Pamene iye anagulitsidwa kwa pafupi zidutswa sate za siliva, uyo anali Yesu. Pamene iye anapangidwa mnyamata wa Potifara, ameneyo anali Yesu. Pamene iye ankakhala pa dzanja lamanja la Farao. Ndipo pamene iye ankachoka, aliyense^lipenga linkalira, ndipo aliyense ankayenera kuti agwade bondo lake, ameneyo anali Yesu. Palibe munthu ankakhoza kubwera kwa Farao kupatula kudzera_kudzera kwa Yosefe; palibe munthu angakhoze kubwera kudzera kwa Mulungu, kokha mwa Yesu yekha. Uyo anali Yesu, Mawu oneneredwa kukhala akukwaniritsidwa, anayankhulidwa mu mithunzi ndi zoyimira. 52 Pamene Yesu anali kuno pa dziko lapansi, Iye anachita chinthu chomwecho chimene aneneri ankachita, ndicho chifukwa iwo anadziwa kuti Iye anali kuwonetseredwa kwa Mulungu kwa Mawu Ake. Izo sizinasowe kuti zitanthauziridwe. 53 Pamene Nataniele anawona izi, iye anagwa pansi, ndipo anati, “Inu ndinu Mfumu ya Israeli, Mwana wa Mulungu, Mfumu ya Israeli. Ife tikukudziwani Inu, palibe munthu angakhoze kuzichita izi.” 54 Nikodimo anabwera ndi usiku, anadzanena chinthu chomwecho mmalo mwa Afarisi. Koma, inu mukuwona, iwo anali omangika kwambiri mu Khonsolo yawo ya Zipembedzo

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

11

kuti iwo sakanakhoza kuzilandira Izo. Iye anafotokoza zimene iwo ankanena, anati, “Rabbi, ife^” “Ife” ndi ndani? Khonsolo yawo! “Ife tikudziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, chifukwa palibe munthu angakhoze kuchita zinthu izi kupatula ngati Mulungu atakhala ndi Iye.” Iwo ankazindikira Izo, iwo ankadziwa kuti Izo zinali, koma iwo okolowekedwa kwambiri mu izo. 55 Ndipo Mulungu, mu zaka forte zapitazo, anagwedeza fuko lino ndi ubatizo wa Mzimu Woyera, ndipo amuna ndi akazi akadali kunja kwa Izo chifukwa iwo amangika mu chinthu chomwecho, akukhala moyo mu chinyezimiro cha tsiku lina. Chavuta ndi chiani? Aliyense akufuna akhale wa Methodisti, wa Baptisti, wa Chipresbateria, wa Chilutera, kapena chinachake. Mukuona, ndi chinyezimiro. 56 Iwo anali akukhala mu chinyezimiro cha tsiku la Mose. Kodi iye ananena chiani? Iye anati^Iwo ankati, “Ife ndife ophunzira a Mose.” 57 Iye anati, “Ngati inu mukadamudziwa Mose, inu mukanandidziwa Ine. Mose analemba za Ine!” 58 Ngati inu mukanamudziwa Lutera, inu mukanaudziwa m’badwo uno! Ngati inu mukanachidziwa chi Methodisti, inu mukanaudziwa m’badwo uno! Pakuti Khristu analemba za m’badwo uno! Mawu amene akukhala akukwaniritsidwa ayenera kuti akhale okwaniritsidwa mu m’badwo uno. Izo sizikusowa winawake kuti azizitanthauzira Izo, Mulungu amachita kutanthauzira Kwake Kwake. Mulungu amazitanthauzira Yekha, chifukwa Iye ali Mmodzi yekhayo yemwe angakhoze kuwatanthauzira Iwo. Malonjezo a Mulungu nthawizonse amatsimikizira zimene Iye ananena, ndipo ndiko kutanthauzira. 59 Tsopano, Yesu, (kuti tisunge nthawi), Yesu ananena, mu Yohane Woyera, mutu wa 14, ndime ya 12, “Iye amene akhulupirira pa Ine, ntchito zimene Ine ndikuchita iye adzazichita nayenso.” Kodi Iye ananena izo? Ndiko kulondola. Izo sizikusowa kutanthauzira kulikonse. Pamene winawake achita ntchito imeneyo, uyo ndi Mulungu. Ndithudi! 60 Iye ananenanso mmenemo, “Monga zinali mu masiku a Loti, chomwechonso zidzakhala ziri pa kudza kwa Mwana wa munthu.” Yesu ananena izo. Kodi Iye ananena izo? Ndithudi, Iye ananena izo! Izo sizikusowa kutanthauzira ayi. Iwo amati, “Chabwino, izo zinkatanthauza^” 61 Izo zinkatanthauza ndendende basi zimene Iye ananena! “Monga zinaliri mu masiku a Loti, chomwecho zidzakhala ziri pa kudza kwa Mwana wa munthu.” Nanga bwanji mu masiku a Loti? Tiyeni tipite mmbuyo kwa mphindi yokha, tikapeze zomwe iwo anali kuchita.

12

MAWU OLANKHULIDWA

62 Panali magulu atatu a anthu mu masiku a Loti: wokhulupirira, wodzipangitsa-kukhulupirira, ndi wosakhulupirira. Alipo mu unyinji uliwonse, chinthu chomwecho. Ife tikupeza kuti Achisodomu anali osakhulupirira. Loti anali wodzipangitsa-kukhulupirira. 63 Abrahamu anali wokhulupirira. Iye anali mmodzi yemwe pangano linatsimikizidwirako. Iye anali mmodzi yemwe anali akuyembekezera mwana wolonjezedwa. Iye anali mmodzi yemwe anali akumuyembekezera iye. Ameni. (Ine sindiri kudzichitira “ameni” ndekha. Ameni amatanthauza “Zikhale chomwecho izo!”) Ndipo ndiko kulondola. Abrahamu sanali mu Sodomu. Abrahamu anali kumtunda ndi kunja kwa Sodomu. Iye ali choimira cha Mpingo wauzimu lero. 64 Loti ndi choimira cha mpingo wa chipembedzo uko mu Sodomu apobe. Penyani, Baibulo linanena kuti, “Machimo a Sodomu anali kusautsa solo yake yolungama tsiku ndi tsiku.” Nchifukwa chiani iye analibe mitsempha yokwanira kuti ayime mozitsutsa izo? Alipo anthu ambiri abwino akhala mu mpingo lero, amayang’ana kunja ndi kumawona akazi atavala zazifupi ndi amuna akuchita zinthu izi, ndi mamembala awo kumapita, kumakasewera gofu Lamlungu, ndi maphwando azibwana, ndi kusambira ndi zinthu, mmalo mosonkhana ku mpingo. Kukhala pakhomo Lachitatu usiku, akuwonera televizioni, mmalo mosonkhana ku tchalitchi. Iwo amamverera ngati kuti anene chinachake icha izo, koma gulu lingawatulutse iwo. Chavuta ndi chiani? Ndi Loti kachiwiri, akuyang’ana kunja pa zenera lake ndi kumawona tchimo, ndipo nkumawopa kulitcha tchimo “tchimo”! 65 Abrahamu sanali mu chisokonezo chawo, iye anali kunja kwa izo. Iye anali choimira cha Mpingo wauzimu. Tsopano penyani zomwe zinachitika pa nthawi yotsiriza pomwe, moto usanagwe kumene. Ndipo awo anali Amitundu. Izo zinali mthunzi wotsogolera moto kugwera pa dziko la Amitundu lero, pamene maufumu ati adzaswedwe ndipo iwo adzawotchedwa. “Miyamba idzakhala pa moto,” atero Ambuye, “ndipo iyo idzayaka ndi kutentha kwakukulu.” Iwo unali mthunzi wa izo. 66 Tsopano tiyeni tiwajambule iwo. Pano pali Abrahamu ali kale kunja, osati mu Sodomu, iye anali kunja kwa Sodomu. Loti anali akadali mu Sodomu. 67 Chinthu chachirendo, mmawa wina wotentha, cha pafupi leveni koloko izo ziyenera kuti zinali, iye anawona amuna atatu akubwera, anthu wamba, akuyenda pansi mu msewu, mkanjira. Abrahamu anali atakhala pansi pa mthundu, akudzipumitsa yekha. Iye anali ali kunja, mwina ndi ziweto mmawa umenewo, anabwerera umo, pafupi dzuwa liri

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

13

paliwombo. Ndipo iye anawona amuna atatu akubwera. Ndipo panali chinachake chokhudza amuna amenewo, chimene, chinaliza belu. O, mai! 68 Nthawizonse pamakhala chinachake chokhudza Mulungu, pamene Izo zibwera pakati pa anthu, Izo zimaliza belu. Iwo amadziwa Izo. Pali chinachake chimene chimawauza iwo, pamakhala kutsimikizira pamenepo. 69 Abrahamu anaathamangira mwamsanga, ndipo anati, “Ambuye wanga, bwerani pafupi ndipo mundirole ine ndikatunge madzi pang’ono, ndikawatenge iwo ndipo ndisambitse mapazi Anu, ndi kukupatsani Inu chidutswa cha mkate, ndiyeno Inu mukhoza kumapitirira pa njira Yanu.” Chotero iye anapatukira uko. Iye anathamangira mu gulu la ziweto ndipo anakagwira mwana wang’ombe ndipo anamupha iye, anamuuza wantchito kuti amusende iye. Anapita mu hema, pansi pake, ndipo anamuuza Sarah kuti akanye ufa wina, apange zina, kapena ufa wina, apange mikate ina, ndi kuti apange mikate pa nkhuti. Anabweretsa izo ndipo anazigawa. Pamene iye anali atakhala pamenepo, akudya, iwo anayamba kuzindikira, Mwamuna uyu ankapitiriza kuyang’ana mmusi chaku Sodomu. Ndipo Iye anati^ 70 Awiri a iwo, kumbukirani, anapita mpaka mu Sodomu. Awiri anapita ku Sodomu. Chonde musati muziphonye izi. Ine ndikulozera ku zomwe Yesu ananena. Awiri a iwo anapita ku Sodomu kuti akabweretseko Loti ndi omwe anali okonzeka kuti atulutsidweko kumusi uko. Ndipo awiri awo amene anapita kumusi uko, anapita uko ndipo anakalalikira. (Ndipo uko kunali Mmodzi yemwe anatsalira mmbuyo ndi Abrahamu. Penyani chizindikiro chimene Iye anachichita.) Iwo anali nacho chizindikiro kumusi uko, uko kunali^Achisodomu anakanthidwa khungu. Kulalikira Uthenga nthawizonse kumachititsa khungu kwa osakhulupirira. Ndipo zindikirani chomwe chinachititsa izo. 71 Tsopano, pali Mmodzi yemwe waima kumbuyo kuno ndipo anachita chizindikiro pamaso pa Abrahamu. 72 Tsopano, kodi inu munayamba mwazindikirapo, wazambiriyakale aliyense, atsatireni Malemba, itsatireni mbiriyakale, sipanayambe pakhala nthawi mu mibadwo ya mpingo pamene munthu anayamba wapita ku mipingo mwa dzina kunja uko mu dziko, kunja uko mu zipembedzo, sikunayambe kwakhala munthu yemwe dzina lake limatsirizira monga Abrahamu, h-a-m, kale. Koma lero iwo ali naye wina, G-r-a-h-a-m. Ndiko kulondola. Akupita kumusi uko, akuwaitanako iwo. Iye akuchita ntchito yodabwitsa nawo. Graham, Billy Graham, wantchito wa Mulungu kunja uko pakati pa zipembedzo, azandale, ndi ena otero, kunsansantha pa izo.

14

MAWU OLANKHULIDWA

73 Tsiku lina pamene iwo ankafuna iye kuti apikisane pa Upurezidenti, iye anazikana izo mosabisa. Mulungu, amudalitse iye chifukwa cha izo. Chifukwa, makampani amowa awo, iye sibwezi atafika ku maziko oyamba monga izo zikanakhalira. Iwo bwezi atataya mabilioni amadola, chifukwa iye akanati awatulutse iwo mulimonse, makampani andudu awo ndi zinthu monga izo. Mukuona, iye ali kunja uko monga mtumiki wa Mulungu kwa Achisodomu. Ndizo ndendende. 74 Koma kumbukirani, panali Mmodzi yemwe anatsalira uko ndi Abrahamu, Mwamuna wina, osati awiri awo amene anapita kumusi uko monga alaliki amakono amene anapita kumusi uko kukalalikira. Zindikirani, uko kunali Mmodzi yemwe anatsalira uko. Awiri anapita kumusi njira iyo, ndipo Mmodzi anatsalira kuno ndi Abrahamu. Ndipo Mmodzi yemwe anatsalira ndi Abrahamu anamupatsa iye chizindikiro. 75 Tsopano penyani, dzina lake linali liri “Abram” ndipo mkazi wake anali ali “Sarai,” tsiku kapena awiri okha izo zisanachitike. Mulungu anali atawonekera kwa iye ndipo anamuuza iye, “Ine ndikukusintha dzina lako tsopano kuchokera pa Abram kukhala Abraham.” (Onani, G-r-a-h-a-m ndi zilembo sikisi, munthu.) Koma A-b-r-a-h-a-m ndi seveni, zilembo seveni; h-a-m, kuthera ndi h-a-m. 76 Tsopano, pamwamba apa mu Mpingo wauzimu, kunali Mmodzi kumtunda uko kwa Abraham, ndipo zindikirani zomwe Iye ananena. Iye anati, “Abraham,” (osati “Abram”) “Abraham, ali kuti mkazi wako” (osati “S-a-r-r-a”) “S-a-r-ah? Ali kuti mkazi wako Sarah?” 77 Penyani zomwe iye ananena, “Iye ali mu hema kuseri kwa Inu.” 78 Ndipo Iye anati, “Ine ndidzakuchezerani inu. Ine ndikuti ndidzakuchezereni inu.” Mukuona puronauni yaumwini, Mmodziyo, molingana ndi lonjezo limene Iye anali atalipanga. Uyo anali Mulungu! Iye anati, “Ine ndikuti ndidzakuchezereni inu.” 79 Ndipo Sarah, (mwa njira yomwe tonse tingamvetsere) anaseka mmwamba mwa malaya ake, kwa iyemwini, iye anati, “Ine, mkazi wokalamba, usinkhu wa zaka handiredi, mbuye wanga” (yemwe anali Abrahamu) “wokalamba nayenso, titadutsa nthawi ya moyo wa izo monga anthu aang’ono.” Anati, “Chifukwa, ife sitingakhoze kukhala ndi zisangalatso monga choncho panonso, ndine wokalamba ndipo iye ndi wokalamba.” Ndipo anati, “Ife sitingakhoze kukhala nazo izo.” Ndipo anati, “Motani? Zinthu izi sizingakhoze kukhala! 80 Ndipo_Mwamunayo (Mulungu mu mnofu waumunthu) anati, “Nchifukwa chiani Sarah waseka ndi kukaikira, ponena zinthu izi?” Mu hema, kumbuyo kwa Ine.

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

15

81 Tsopano penyani, ngati iwo suli utumiki womwewo umene Yesu Khristu anali nawo! Iye anayang’ana apo pa omvetsera ndipo anazindikira malingaliro awo. Iye anamuuza Petro yemwe iye anali ndi chomwe dzina la abambo ake linali. Anamuuza Natanieli. 82 Anamuuza mkazi pa chitsime, pamene iye anati^Iye anati, “Pita ukanditungire Ine akumwa,” kapena “Ndibweretsere Ine akumwa.” 83 Iye anati, “Bwana, si mwambo wake kuti Inu muziyankhula kwa^inu Ayuda kuyankhula kwa Asamaria. Ife tiribe chochita kwa wina ndi mzake.” 84 Iye anati, “Koma ngati iwe ukanadziwa Yemwe iwe ukuyankhula naye, iwe ukanandipempha Ine akumwa.” Kuyankhulanako kunapitirira. Iye anati, “Pita ukamutenge mwamuna wako ndipo ubwere kuno.” Iye anati, “Ine ndiribe mwamuna.” Iye anati, “Iwe wanena bwino, pakuti iwe unali nawo asanu.” Iye anati, “Bwana!” 85 Tayang’anani pa kusiyana pakati pa iye ndi iwo_ndi ansembe aja a tsiku ilo, khonsolo lija likukhala mwa chinyezimiro cha tsiku lina. Iwo ankati, “Uyu ndi Mdierekezi!” Iwo ankayenera kukayankhira kwa gulu lawo chinachake, chifukwa ilo linkasowa icho. 86 Koma nchiani chimene mkazi wamng’ono wosauka uyu, Mbewu yokonzedweratu ija itagona mu mtima wake^Iye anali atadwala ndi kutopa ndi zinthu zimenezo, iye anali atapita pa misewu monga wachiwerewere. Koma pamene iye anachiwona Icho, iye anati, “Bwana, ine ndazindikira kuti Inu ndinu Mneneri. Ife sitinakhalepo naye mmodzi kwa zaka foro handiredi, ndipo ife tinauzidwa kuti pamene Mesiya adzadza ndizo zinthu zomwe Iye ati adzachite.” O, mai! Mbewu ija itagona mmenemo inadumphira ku moyo! Chifukwa? Izo sizinkasowa kutanthauzira ayi. 87 Yesu anati, “Ine ndine Iye amene akuyankhula kwa iwe.” Izo sizinasowe kutanthauzira ayi. Iye anali atachita chozizwitsa ndipo anali atachitira umboni kuti Iye anali Mesiya ameneyo, ameni, ndipo anali ndi umboni wa ndendende pa zomwe Mulungu anali atalonjeza (“Ambuye Mulungu wanu adzautsa Mneneri wonga ine,” anatero Mose). Chinali chiani icho? Kutsimikizira kwa Lemba! 88 Iye anathamangira mu mzinda, ndipo anati, “Bwerani, mudzamuwone Mwamuna Yemwe wandiuza ine zinthu zomwe ndazichita. Kodi uyu si Khristu yemwe? Kodi uyu si Iyeyo? Iye wandiuza ine zimene ine ndinazichita.”

16

MAWU OLANKHULIDWA

89 Tsopano zindikirani, Yesu, ameneyo anali Iye kumtunda uko mwa Munthu ameneyo yemwe anali atatembenuzira msana Wake ku hema ndi kumuuza Sarah zomwe anali kuziganiza mkati mwa hema. 90 Mawu a Mulungu amati, mu Ahebri, mutu wa 4, kuti^Iye amanena izi, “Mawu a Mulungu ndi amphamvu kwambiri ndi akuthwa kuposa lupanga la konsekonse, odula mpaka mkati mwa mafuta a mmafupa, ndi ozindikira maganizo ndi zolinga za mtima.” Ndiwo Mawu! Ndipo nthawi iliyonse pamene mneneri anabwera, iye amabwera ndi Mawu, ndipo iye anali Mawu a m’badwo umenewo. Ndipo kodi iwo ankachita chiani? Wonenera yemwe ankazindikira maganizo amene anali mu mtima. 91 Iwo anachitapo izo mwa Yesu Khristu chifukwa Iye anali chidzalo cha Mawu. 92 Ndipo Yesu anati, “Monga zinaliri mu masiku a Sodomu, chomwecho zidzakhala ziri mu kudza kwa Mwana wa munthu.” Mzimu wa Mulungu ukanadzabwera pa dziko lapansi mu mawonekedwe a anthu okhalapo, Mulungu atawonetseredwa mu mnofu wa umunthu (Ameni! Kodi inu mukuziona izo?), ndipo akanadzachita chinthu chomwecho chimene Mulungu anachichita mu mnofu wa umunthu ku Sodomu. Kumbikirani, iwo anali akuyembekezera mwana wolonjezedwa. Ndipo, zitachitika kumene izo, mwana wolonjezedwayo anabwera. Icho chinali chizindikiro chotsiriza chimene Sodomu ndi gulu la Abrahamu linachiwona mwana wolonjezedwayo asanafike. Kodi inu munazindikira izo? Ndipo tsopano Mpingo wauzimu wafika pa ora limenelo. 93 Winawake akuti, “M’bale Branham, kodi inu munati ‘uyo anali Mulungu’?” 94 Baibulo linati, Uyo anali Mulungu! Izo sizikusowa kutanthauzira. Iye ndi Elohim. Ndicho chimene Abrahamu anamutcha Iye. Wowerenga Baibulo aliyense amadziwa izo. Elohim, “Mmodzi wokwana-mzonse.” Iye anali Woyamba, Wotsiriza; Chiyambi, Mapeto. Elohim! Abrahamu anamutcha Iye “Elohim.” Mulungu (mu zilembo zazikulu mu Chihebri), Elohim; basi monga pa chiyambi, “Mulungu,” Elohim. 95 Iye anali Elohim atawonetseredwa mu mnofu wa umunthu, atavala zovala za umunthu, akudya chakudya cha umunthu. Ameni! Chizindikiro kuti mu masiku otsiriza kuti Mulungu adzawonekera kachiwiri pakati pa anthu Ake mu mnofu wa umunthu! Ameni! Yesu anati, “Ntchito zimene Ine ndikuzichita inunso mudzazichita. Ndipo monga zinaliri mu masiku a Sodomu, chomwechonso izo zidzakhala pa kudza kwa Mwana wa munthu.” Ameni! Izo sizikusowa kutanthauzira ayi; izo zikusowa kuwonetseredwa, ndicho chomwe izo zikusowa. Ameni. Kodi inu mukukhulupirira izo?

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

17

Tiyeni tiweramitse mitu yathu. 96 Atate athu Akumwamba, ife tikupereka kwa Inu lonjezo Lanu usikuuno lomwe Inu munati zinthu izi. Inu munazilonjeza izo. Palibe wina yemwe angakhoze kuwapangitsa Mawu Anu kukhala amoyo koma Inu. Inu munati, “Pakhale kuwala,” ndipo panali kuwala. Palibe mmodzi yemwe ayenera kuzitanthauzira izo, izo zinawonetseredwa. 97 Monga ife tinamubwerezera Yesaya, mneneri, “Namwali adzaima,” iye anatero; sizikusowa kuwonetsera kulikonse, iye anachita izo. Ndizo zomwe zinachitika. 98 Inu munati, pamene Iye adzabwera Iye adzabadwira mu Betelehemu, “Kuchokera mu Betelehemu, Yudea. Kodi sindiwe wamng’ono pakati pa akalonga onse a Yuda, a Israeli? Koma kuchokera mwa iwe mudzabwera Wolamulira wa anthu Anga.” 99 Zinthu zimene Iye akanadzachita, zimene Iye akanati adzalire pa mtanda, momwe Iye akanati adzatsutsidwe, kupyozedwa mapazi Ake ndi manja Ake, “Iye anavulazidwa chifukwa cha zolakwa zathu, ndipo anatunduzidwa chifukwa cha kusaweruzika kwathu; chilango cha mtendere wathu chinali pa Iye; ndi mikwingirima Yake ife tinachiritsidwa.” 100 Momwe kuti Davide anati, “Ine sindidzasiya moyo Wake mu hade, ngakhale kuti sindidzalola Woyera Wanga kuti awone chivundi.” Ndipo pa tsiku lachitatu maora sevente thuu asanakwanire kuti zivunditse thupi Lake, Mawu a Mulungu anati, “Iye adzawuka.” (Iwo anati iwo anabamo thupi Lake; iwo akukhulupirirabe izo.) Koma ife tikukhulupirira, Ambuye, Mawu Anu! Izo zinawonetseredwa. Yesu Khristu anawuka ndipo Iye anati, “Ine ndi^Taonani, Ine ndiri ndi inu nthawizonse, ngakhale mpaka ku mapeto a dziko.” 101 Ife tikukhulupirira kuti Inu muli pano usikuuno. Ife tikukhulupirira kuti Inu muli basi mochuluka Yesu Khristu usikuuno, pano, monga Inu munaliri konse. Ndipo Inu mukungofuna maso, mikono, miyendo, kamwa, miyoyo, matupi, zomwe Inu mungakhoze kuzigwiritsa ntchito kuti mudziwonetseremo Nokha. Mulungu, tiyeretseni ife usikuuno, kuti ife tikhoze kumamuwona Yesu Khristu wamoyo ali moyo pakati pathu. Muloleni Iye abwere! Ndiye zidzafika pochitika, monga njala ya Agriki aja amene anabwera tsiku lijali, ndipo anati, “Bwana, ife tikanafuna timuwone Yesu.” Ndipo iwo anafika pomuwona Iye. O, momwe kukondweretsa kwake kuyenera kuti kunali pamene iwo anayang’ana pa Iye! 102 Mulungu, Ndinu yemweyo lero. Ndipo Inu munalonjeza kuti ngati ife tichita njala ife tikhoza kukuonani Inu. “Kanthawi pang’ono, ndipo dziko silindiwona Ine” (osakhulupirira); “komabe inu mudzandiwona Ine, pakuti Ine

18

MAWU OLANKHULIDWA

ndidzakhala ndi inu, ngakhale mkati mwanu, mpaka kumathero a dziko.” Ife tikudziwa kuti Ndinu yemweyo dzulo, lero, ndi kwanthawizonse. 103 Ambuye, Mawu anenedwa kale, iwo alembedwa kale, tsopano muwalole iwo achitidwe, kwa Ulemerero wa Mulungu, kuti zisonyeze kuti Iye amasunga Mawu Ake. Ameni. Mulungu akudalitseni inu. 104 Ine ndikuti ndiyitane mzere wa pemphero. Ine ndikukhulupirira Billy anati iye anapereka makadi a pemphero, wani mpaka handiredi, kapena chinachake monga choncho. Iye sali pano pakali pano. Ndi^Nambala ya khadi lapemphero ndi chiani^Winawake ayang’ane kuseri kwa yanu^Iyo inga_iyo ingakhale nambala ndi_chilembo (A,B,C,D, kapena^). Ndi chiani izo, A? Chabwino. 105 Tiyeni tikhale ndi A, nambala wani, thuu, firii, foro, faifi. Ingoyambani kuima monga choncho. A, nambala wani, nambala thuu, nambala firii, nambala foro. Foro, ine sindinawone iyo akuimirira. Khadi la pemphero nambala foro. Wani, thuu, firii. Pemphero^Mwinamwake iwo sangakhoze kudzuka. Ngati iwo sangakhoze, winawake ayang’ane pa khadi la woyandikana naye, iye akhoza kukhala ndi khadi ndipo iye sakukhoza kuima. Mwamsanga tsopano. Ndi izo apo, foro. Faifi, khadi la pemphero nambala faifi, sikisi, seveni, eyiti, naini, teni, leveni, thwelofu. Ingoyambani kumabwera kuno tsopano pamene manambala anu akuitanidwa. Nambala wani, thuu, firii, zingomabwerani kuno podzera uku. Khadi la pemphero nambala wani, thuu, firii, foro, faifi, sikisi, seveni, eyiti, naini, teni, leveni, ingotengani malo anu. Leveni, thwelofu, satini, fortini, fifitini, sikisitini, seventini, eyitini, naintini, twente, twente wani, twente thuu, twente firii, twente foro, twente faifi. Pali aliyense yemwe sangakhoze^ 106 Ine ndikumuwona mwamuna wamng’ono mu chikuku kumbuyo uko. Ngati nambala yako iitanidwa, mwananga, ndi_ndipo ngati iwe sungakhoze kufika^chabwino, ingokweza dzanja lako, ife tiwona kuti iwe ufike kuno. Ukuona? 107 Ndi angati muno alibe khadi la pemphero ndipo komabe inu mukudwala? Tiyeni tiwone manja anu, paliponse. Pomwe pano, ndiko kulondola, ikani manja anu mmwamba. Kodi inu mukukhulupirira? Pamene akuwatengera awo palimodzi, kodi inu mukukhulupirira Izi, kuti Iye ali yemweyo dzulo, ndi kwanthawizonse? Ndi angati? Penyani izi atumiki; kodi Lemba silimanena lero, abale, kuti Iye ndi Wansembe Wamkulu yemwe akhoza kukhudzidwa ndi kumverera kwa zifooko zathu? Si kulondola uko? Ndi angati akukhulupirira izo, kwezani dzanja lanu? Iye ndi Wansembe Wamkulu yemwe akhoza kukhudzidwa ndi kumverera kwa zifooko zathu.

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

19

108 Ndiye ngati Baibulo likuti, “Iye ali yemweyo dzulo, ndi kwanthawizonse,” ndi angati akuzikhulupirira izo? Ndiye kodi Iye akanati azichita motani lero? Iye akanayenera kuti azichita monga Iye anachitira dzulo. Ndi kulondola uko? Kodi Iye ali kuti usikuuno? Akukhala pa dzanja lamanja la Ufumu, thupi Lake; Mzimu Woyera uli kuno mu nyumba muno, kuti uzimupangitsa Iye kudziwika. 109 Zindikirani, tsopano yang’anani. Chinachitika nchiani pamene winawake anagwira chovala Chake mmbuyo uko, mkazi tsiku lina? Iye anali alibe khadi la pemphero, ife tikanati titi, koma iye anagwira chovala Chake. Ndipo pamene iye anagwira chovala Chake, Yesu anapotoloka apo ndipo anati, “Ndani wandigwira Ine?” 110 Petro anamudzudzula Iye, ndipo anati, “Bwanji, Ambuye, izo sizikumveka ngati zoganiza bwino basi. Bwanji, aliyense akuyesera kuti akugwireni Inu. Bwanji mukuti, ‘Ndani wandigwira Ine?’ ” 111 Iye anati, “Koma Ine ndikuwona kuti Ine ndafooka.” Ndi angati akudziwa izo? Ukoma, chimene chimatanthauza “mphamvu,” unachoka mwa Iye. “Ine ndafooka, wina wandigwira Ine ndi mtundu wina wa magwiridwe.” Ndipo Iye anapotoloka ndipo anayang’ana kwa omvera mpaka Iye anapeza pamene mpita uwo wa chikhulupiriro unali. 112 Aliyense anali akuika mikono yawo momukumbatira Iye, “O Rabbi, ife tikukukhulupirirani Inu,” ndi zonse izi. 113 Koma panali wina yemwe anakhulupirira kwenikweni Izo. Ndipo iye anagwira chovala Chake ndipo anakhulupirira kuti iye anachiritsidwa, chifukwa iye ananena mu mtima mwake ngati iye akanachita izo ndi chomwe chikanati chichitike. 114 Iye anatembenuka apo ndipo anayang’ana pa omvetsera mpaka Iye anamupeza iye, ndipo Iye anati^anamuuza iye vuto lake la magazi linali litasiya ndipo iye anachiritsidwa. Ndi kulondola uko? Tsopano, ndi momwe Iye ankachitira, mwa anthu omvetsera. 115 Tsopano, Ine ndikudzinenera kuti Iye si wakufa, Iye ali basi wamoyo mochuluka lero monga Iye anakhala ali. Ndipo Baibulo linati, Yesu anati, Mwiniwake, “Monga zinali mu masiku a Sodomu, chomwecho zidzakhala ziri mu kudza kwa Mwana wa munthu.” 116 Tsopano tayang’anani, ziribe kanthu mtundu wa mphatso yomwe Mulungu ali nayo pamwamba pano, payenera kukhala mmodzi pansi, aponso, kuti ayankhire kwa iyo. Iye anapita mu mzinda, Baibulo limati, “Panali zinthu zambiri zimene Iye sakanakhoza kuzichita chifukwa cha kusakhulupirira kwawo.” Ndi kulondola uko? Chinthu chomwecho lero. Inu

20

MAWU OLANKHULIDWA

muyenera kuti muzimukhulupirira Iye. Inu mukuyenera basi kuti muzimukhulupirira Iye. Ndi njira yokha yomwe inu mungathere. 117 Kodi mzere wa pemphero wakonzeka? Tsopano, aliyense molemekeza kwa pafupi maminiti teni okha. Sindikudziwa ngati nditi ndifikeko, ine ndiri nawo pafupi twente-faifi kapena sate ayima apo. Koma tsopano, mu mzere wa pemphero, mmodzi aliyense wa inu kunja uko mu mzere wa pemphero yemwe akudziwa kuti ndine mlendo kwa inu, ndipo ine sindikudziwa kanthu za inu, kwezani mmwamba dzanja lanu. Mmodzi aliyense mu mzere wa pemphero. 118 Tsopano kunja mwa omvetsera, amene akudziwa kuti ine sindikudziwa kanthu za inu, kwezani mmwamba dzanja lanu. Mwaona? Tsopano, tsopano, ichi ndi chimene ine ndikuyesera kuti ndinene, mzanga, ona. Tsopano, ndi izi. Atumiki onse awa kuno ku nsanja. Ndipo Khristu anapanga lonjezo ili. Mwaona, izo zinalembedwa kale. Ndi liti pamene ziri zoti zidzachitike? Mu masiku otsiriza, kusanachitike kumene Kudza kwa Ambuye. Ndi kulondola uko? Izo zinali zoti zidzafike pochitika pamenepo. 119 Tsopano, ndiwo Mawu amene ananeneredwa lero. Osati kuwala kwa Lutera; osati kuwala kwa Wesile; ndipo osati ngakhale kuwala kwa Chipentekoste. Iko kunapita kale pa msewu tsopano. Tsopano, kwa Lutera nkwabwino; kwa Methodisti ndi kwabwino; kwa Baptisti ndi kwabwino; onse a iwo, Chipentekoste, nkwabwino. Alipo amitundu yonse amene ali pano usikuuno. Izo si_izo si_izo si anthu pawokha. Bwanji ngati^ 120 Iwe sungakhoze konse kumuuza wa Methodisti chirichonse cha Lutera, chifukwa iye amakhulupirira mu kuyeretsedwa ndipo Lutera satero. Mwaona? 121 Iwe sumamuwuza konse wa Pentekoste kuti “kuyeretsedwa ndi zonse zake,” iye waona kubwezeretsa kwa mphatso. Iye sati akhulupirire izo. Ayi, iye ali nazo zoposa izo. Mwaona? Ndipo ndiwo m’badwo wa mpingo wotsiriza umene ife tinali nawo, ndipo Baibulo limati sipadzakhala mibadwo ya mpingo inanso. 122 Koma panayenera kukhala pali kusonkhana kwa anthu, mukuona, ndipo ndife pano. Tsopano, kumbukirani, chizindikiro chotsiriza. Kodi ife anthu tikuyang’anira mwana wolonjezedwa? Kwezani mmwamba dzanja lanu. Kodi inu mukukhulupirira kuti ndinu Mbewu ya Abrahamu pokhala muli mwa Khristu? Kwezani mmwamba dzanja lanu. Ndiye, Mbewu ya Abrahamu, landirani chizindikiro chanu! Icho sichiri kunja mu Babeloni, icho sichiri kunja uko mu dziko la zipembedzo. Icho chiri pano pakati pa inu, omwe sali mu chisokonezeko icho kunja uko. Mukhulupirire izo!

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

21

123 Pano pali mkazi, iye ndi mlendo kwathunthu kwa ine, penapake pafupi usinkhu wofanana. Ine sindinamuwonepo konse mkaziyu mu moyo wanga. Ngati ine ndingakhoze kumuchiritsa mkazi uyo ine ndikanachita izo, ngati iye akudwala. Ine sindikudziwa kanthu za iye. Kodi inu munamuwona iye akukweza dzanja lake maminiti angapo apitawo. Ine_ine sindinamuwone iye. Iye wangokhala mkazi basi atayima apo. 124 Lero iwo anabwera kuno ndipo anabweretsa mulu wa makadi a pemphero, anawasakaniza iwo ndi kuwapereka kwa anthu. Wina anatenga nambala wani pano, ndi nambala teni kumbuyo uko, nambala fifitini, nambala seveni, nambala^basi monga choncho. Iwo onse atasakanizidwa, patsogolo panu pomwe, tsiku lirilonse. Ndipo pamene iwo aitanidwa, iwo amangoitanidwa onse mozungulira kuchokera paliponse. Mwaona? Ndipo, tsopano, inu simukusowa ngakhale kukhala nalo khadi la pemphero, ingokhalani pamenepo ndi kukhulupirira. Bwanji osati^ 125 Dzitsineni nokha, usikuuno, mupeze ora limene tiri kukhalamo. Mwaona? Tsopano, yangotsala pafupi kutha, nayonso, mzanga. Yangotsala pafupi kutha! 126 Tsopano, ngati Mulungu wa Abrahamu anamuukitsa Yesu Khristu kuchokera kwa akufa, ndipo Yesu ameneyo analonjeza kuti mu masiku otsiriza zizindikiro zomwezo zimene Abrahamu^zimene Mngelo (yemwe anali Mulungu mu mnofu waumunthu) anachita pamaso pa Abrahamu, mwana wolonjezedwa asanafike kumene, Yesu anati chinthu chomwecho chidzachitika lero. 127 Tsopano, ife tikuwona mizinga ndi zipembedzo, ndi zonse izo, ndi chisokonezo chimene iwo alimo. Ife tikumuona Billy Graham uko kutali, ndi Oral Roberts, ndi anthu onse awo kunja uko; mtumiki wa Chipentekoste ndi mtumiki wa chipembedzo kumusi uko, ife tikuona zonse izo zikupitirira, akuchita chizindikiro. Billy Graham, wazamulungu mpaka ku dontho, zomwe chipembedzo chimakhulupiriramo. Oral Roberts, mchiritsi mpaka ku dontho, ndendende basi chimene Chipentekoste^ 128 Koma tayang’anani kuno, kuli chinachakenso chinalonjezedwa kwa Mbewu ya Abrahamu. Uko iwo ali uko pakati pa zipembedzo izo; pali chinachake kunja kwa zipembedzo chimene chiyenera kuti chizichitika, kusonkhanitsa anthu. Ife tizisiya izo zipite mpaka mawa usiku. 129 Penyani, ine sindikumudziwa mkazi uyo. Ine nditembenuzira nsana wanga kwa iye. Ngati Ambuye Mulungu ati anene chinachake kwa mkazi ameneyo, mwina ndi_ndi zapabanja, mwina ndi zachuma, mwina akudwala; ine sindikudziwa. Iye adziwa ngati ziri zoona kapena ayi.

22

MAWU OLANKHULIDWA

130 Ngati Iye ati achite chinthu chomwecho usikuuno chimene Iye anachichita apo, kodi inu mumukhulupirira Mulungu yemwe Yesu Khristu analonjeza kuti akanadzakhala pano mu masiku otsiriza? Ndi angati akukhulupirira kuti ife tikukhala monga mu Sodomu, pamene dziko lonse lapita mu chikhalidwe cha Chisodomu? Ndi angati a inu mukukhulupirira zimene ine ndakuuzani inu usikuuno kuti ndi Choonadi? Ndiye, ana ndi Mbewu ya Abrahamu, khulupirirani Mulungu! 131 Tsopano, chotero kuti zifike ku malingaliro anu kuti ine ndikuyesera kuti ndinene chinachake kwa mkazi, kumuyang’ana iye mu nkhope, kapena kutenga zinthu zonse za kuwerenga maganizo kapena chirichonse chimene inu mukufuna kuti mudziwe. Aliyense amene amadziwa za kuwerenga maganizo ayenera kukhala ndi kulingalira kwabwino kuposa zimenezo. Mwaona? Mwaona? Kodi inu munayamba mwamuwona wowerenga maganizo akulalikira Uthenga? Kodi inu munayamba mwamuwona wazamizimu akulalikira Uthenga, akuchita zizindikiro ndi zodabwitsa, kumati Yesu Khristu ali yemweyo? Ayi. 132 Mwaona, ndizo basi^ndi malingaliro a anthu. Mwaona, iwo ndi akhungu. Kodi inu mukukhulupirira kuti iwo akhoza kukhala akhungu? Baibulo linati iwo akanati adzakhale. Ndi kulondola uko? “Ammutu, amalingaliro apamwamba, okonda zosangalatsa kuposa kukonda Mulungu, okuswa chigwirizano, onenera zabodza, osadzigwira, onyoza iwo amene ali abwino, okhala nawo maonekedwe aumulungu, koma nkumakana Mphamvu yake.” 133 Kodi Yesu sananene, mu Mateyu Woyera 24:24, kuti “Mizimu iwiriyo mu masiku otsiriza ikanakhala pafupi kuti inyenge Osankhidwa omwe, ngati kukanakhala kotheka”? Koma si kotheka. Iwo anali mu malingaliro a Mulungu pa chiyambi, ndipo iwo ali gawo la Mulungu. 134 Tsopano, Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi Yakobo, mulole izi zidziwike usikuuno kuti ine ndikunena Choonadi za Inu. Ndi Inuyo, Ambuye. Modzichepetsa mulole antchito Anu akhale okhoza kuchotsa malingaliro awo mu njira, kuti Inu muzikhoza kuwagwiritsa ntchito matupi athu kwa Ulemerero Wanu. Mu Dzina la Yesu, Mwana wa Mulungu. Ameni. 135 Kodi mphatso ndi chiani? Osati chinachake chimene iwe umachitenga ndi kuchiwaza ndi kuchitembenuza. Ayi, ayi. Ndiko kudziwa kudzichotsa wekha panjira kuti Mulungu azikhoza kukugwiritsa iwe ntchito. Mphatso ndi iweyo kudzichotsapo basi, ndiye Mulungu amaigwiritsa ntchito iyo. 136 Dona kumbuyo kwa ine afa pomwe pano ngati iye sachiritsidwa. Dona kumbuyo kwanga wangopemphereredwa kumene ndi mwamuna wina, posachedwapa. Iye ali ndi khansara. Khansara ili mu bele lake ndiponso mu mapapu ake.

23

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

Ndipo iye anangopemphereredwa posachedwapa, ndipo iye akuyesa kuti avomereze izo mwa chikhulupiriro kuti iye wachiritsidwa. Ndizo PAKUTI ATERO AMBUYE! Kodi izo nzoona, dona? [Donayo akuti, “Inde, izo zedi ndi zoona.”_Mkonzi.] Ngati izo ziri, gwedezani_gwedezani dzanja lanu kwa omvetsera. Mulungu wa Abrahamu akadali moyo! Chabwino, pitani mukukhulupirira zimene inu mwakhulupirira ndipo inu mukakhala bwino. Ameni. Inu mukukhulupirira? omvetsera awo?”

Inu

mukuti,

“Nanga

bwanji

137 Mkazi uyu amene wakhala pano ndi yake^pa mapeto a mzere, dona wachiwiri apo pomwe. Pamene ine ndinatembenuka mozungulira pomwepo ine ndinawona chinachake, chinthu mozungulira mkono wake, kuthamanga kwa magazi kukupopa. Iye ali ndi kuthamanga kwambiri kwa magazi. Ndi kulondola uko, dona? Kwezani mmwamba dzanja lanu. Ngati inu mukukhulupirira, kuthamanga kwa magazi kwanu kutsika pansi. Mulungu wa Abrahamu akadali powonekera pano. Iye ali basi ndendende chimene icho chinali, Mawu a Mulungu a tsiku lino! 138 Inu muli bwanji? Inu mukukhulupirira tsopano? Khalani nacho chikhulupiriro mwa Mulungu! Amawoneka ngati kuti ndi mwana chabe. Mulungu akudziwa mtima wako, dona wamng’ono, ine sindikudziwa. Kodi iwe ukukhulupirira kuti Mulungu ndi wokhoza kuwululira kwa ine chimene chiri cholakwika? Kodi iwe umukhulupirira Iye ngati ine nditero? Si za iwe, ndi za winawakenso, uyo ndi m’bale wako. Ndipo iye wodwalika kwambiri ndipo iye ali mu mzinda kumpoto kwa kuno, Tulare. Ndipo iye ali mu chipatala ndipo iye ali ndi leukemia, ndipo madokotala amulephera iye kuti afe. Palibe ziyembekezo nkomwe. Ndiko kulondola. Kodi iwe ukukhulupirira? [Donayo, akulira, nayankha, “Inde.”_Mkonzi.] Chabwino. Uli ndi chiani mdzanja lako? Tenga icho ndipo kachiyike icho pa iye. Ndipo usati ukaikire za izo. Khulupirira! Ameni. 139 Kodi inu mukukhulupirira? Ine sindinayambe ndamuwonapo donayo mu moyo wanga. Koma Mulungu akadali Mulungu! Tsopano, ndiwuzeni ine munthu yemwe angakhoze kuchita izo? Izo siziri mu kapangidwe ka munthu kuti azichita izo. Ndi Mulungu yemwe Yesu Khristu analonjeza kuti akanadzakhala kuno mu masiku otsiriza ndipo akanadzadzitsimikizira Yekha (pamaso pa Mbewu ya Abrahamu pomwe) monga izo zinaliri mu masiku a Sodomu. 140 Tsopano pano, ine sindikumudziwa donayu, ndife alendo kwa wina ndi mzake, ine ndikuganiza nthawi yathu yoyamba kukomana mu moyo. Kodi inu mukundikhulupirira ine kuti ndine wantchito Wake? Kodi inu mukukhulupirira izi kuti ndi

24

MAWU OLANKHULIDWA

Mawu? Ndipo inu mukudziwa kuti ngati^Mawu awa akadali ozindikira maganizo ndi zolinga za mu mtima. Ndi kulondola uko? Mawu ndi Mchiritsi, naponso, ngati inu mungati muwakhulupirire Iwo. Inu mukutero? Inu mwaphimbidwa, inunso, ndi mthunzi wakuda. Ndi khansara. Ndipo inu mukukhulupirira kuti Mulungu akhoza kundiuza ine pamene khansara imeneyo ili? Iyo ili mu matumbo a mmusi, adokotala ananena chomwecho. Kodi inu mukukhulupirira tsopano kuti inu muchiritsidwa? Pitani, ndipo musati mukaikire nkomwe, ndipo Mulungu akakukhalitsani inu bwino. Ameni. 141 Inu mukukhulupirira, aliyense? Ndendende basi zimene Iye analonjeza kuti adzachita! Khalani nacho chikhulupiriro mwa Mulungu, musati muzikaika. 142 Ndife alendo kwa wina ndi mzake. Ine sindikukudziwani inu. Ngati tiri alendo, aloleni omvetsera adziwe izo, ife titagwirana manja athu. Ine sindinayambe ndamuwona mkaziyu mu moyo wanga. 143 Kodi inu mukukhulupirira kunja uko? Inu mukukhulupirira kuti ndi Yesu Khristu? Ndi chiani ichi? Ndi Mawu Ake. Pamene anthu awa akukana Iwo, iwo sakumukana munthu, iwo akuwakana Mawu. Ndi Mawu amene anali kunja, samakhoza kubwerera mkati. 144 Tsopano, donayo ndi mlendo kwa ine. Ine sindinayambe ndamuwonapo iye mu moyo wanga. Mulungu ndi mchiritsi. Izo zikhoza kusakhala za machiritso, zikhoza kukhala za chinachake, koma ngati Mulungu angafotokoze kwa ine lomwe liri vuto lanu, kodi inu mungati mundikhulupirire ine? Chinthu choyamba chimene inu mukufunira pemphero, ndicho, inu muli ndi khutu loyipa. Limodzi la makutu anu, inu simukukhoza kumva ndi ilo. Ndiko kulondola. Ndizo zoona. Ndiyeno inu muli ndi chizolowezi, ndipo inu mukufuna kuti muthane nacho chizolowezi chimenecho, ndicho kusuta ndudu. Ikani chala chanu mu khutu lanu labwino tsopano, chabwino, khutu lanu labwino. Chabwino. Tsopano khulupirirani Mulungu ndipo zipitani pa njira yanu, ndipo musati^ndipo inu simukasuta kenanso nduduzo ngati inu muti mukhulupirire. Pitani, ndipo Ambuye akudalitseni inu. Inu mukuona chimene chachitika. Kodi Iye si weniweni? 145 Ine sindikukudziwani inu, ndife alendo kwa wina ndi mzake. Ine sindinayambe ndakuwonanipo inu mu moyo wanga, koma Mulungu akukudziwani inu. Ngati Mulungu angakhoze kundiuza ine chinachake cha inu, kodi inu mungati mukhulupirire? 146 Kodi omvera onse angakhulupirire? Alipo wina kunja uko akumudziwa mkaziyu? Aliyense mwa omvera akumudziwa mkaziyu? Chabwino, inu mudziwa ngati izi ziri zoona kapena ayi. Izi ziyenera kukhazikitsa. Izi ziyenera kunena choonadi.

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

25

147 Tsopano inu mukukhoza kuwona zimene zinachitika basi mu maminiti angapo apitawo. Mukuona? Izo zangokhala kuti^Ine ndikuzandima. Mukuona? Izo kungoti chirichonse chikukhala mwakhungu kwa ine. Mwaona, Ndiko kuzindikira za mu mtima. Mwaona, Iwo ndi Mzimu Woyera. Si ine. Ndi Mawu olonjezedwera tsiku lino. Izi sizinayambe zakhalapo chiyambireni masiku a atumwi, izo sizinayambe zakhalapo. Koma pamene izo zinanenedwa, “Kusanachitike kumene kudza kwa Mwana wa munthu. Monga zinaliri mu masiku a Loti, chomwecho izo zidzakhala ziri mu kudza kwa Mwana wa munthu.” Osakhulupirira sakukhulupirira Izo. Iwo sali kuyembekezeredwa kuti azikhulupirire Izo. Koma okhulupirira akuzikhulupirira Izi! 148 Tsopano, ngati Mzimu Woyera uti uwulule izi, ndi angati amene ati akhulupirire ndi mtima wanu wonse, inu kwezani dzanja lanu? 149 Inu muli ndi kuwonongeka. Inu munali ndi ngozi ya galimoto, iyo yakoka timafupa tofewa nkumasuka pa khosi panu. Ndipo inu mulinso ndi impso yokokedwa nkumasuka. Uko nkulondola, si choncho? Inu mukukhulupirira? Inu mukhala bwino bwino. Ambuye alemekezeke. 150 Inu mukukhulupirira kuti Mulungu amachiza vuto la impso? Ndiye pitirirani ndipo landirani machiritso anu. 151 Bwerani, dona. Yang’anani mbali iyi. Inu mukukhulupirira kuti Mulungu amachiritsa vuto la mtima? Chabwino, pitani pa msewu wanu ndipo khulupirirani, ndipo mtima wanu ukhala bwino bwino. 152 Bwerani pano. Inu mukukhulupirira Mulungu akhoza kuchiza nsana wanu, kukukhalitsani inu bwino? Pitirirani ndipo zikakhulupirirani izo ndiye. Zingokhulupirirani Mulungu, ndizo zonse zimene inu muyenera kuti muzichita! 153 Bwerani, dona. Inu mukukhulupirira Mulungu akhoza kuchiza vuto la mmimba? Pitani, mukadye mgonero wanu, mukhulupirire ndi mtima wanu wonse. 154 Bwerani. Inu mukukhulupirira Mulungu akhoza kuchiza nyamakazi? Ndiye zipitani, mukukhulupirira, ndipo akupangani^ndipo Mulungu akukhalitsani inu bwino. 155 Chabwino, bwerani. Inu mukukhulupirira ndi mtima wanu wonse? Inu mukukhulupirira? Nyamakazi, kachiwiri. Kodi inu mukukhulupirira kuti Mulungu akhoza kukukhalitsani inu bwino? Zipitani, mukukhulupirira Izo, nkuti, “Zikomo Inu, Ambuye.” Ndi angati akukhulupirira kunja uko? Kodi inu mukukhulupirira?

26

MAWU OLANKHULIDWA

156 Dona wakhala apayu amene atavala diresi yofiira, amene akukweza mmwamba dzanja lake pomwepa, akuvutika ndi kuthamanga kwa magazi. Inu mukukhulupirira Mulungu akhoza angakukhalitseni inu bwino? Inu mukutero? Chabwino. Ikani manja anu pa dona uyo pafupi ndi inu pamusi apo, ndipo mumuuze iye kuti liwu lake likhala bwino bwino. Ameni. Ndi izo apo. Ameni. Kodi inu mukukhulupirira? Khalani nacho chikhulupiriro! 157 Apa pali bambo wakhala pano, iye ali ndi kutaya kwa magazi. Kodi inu mukukhulupirira, bwana, mwakhala pomwe pano? Inde, inu muli ndi kutaya kwa magazi. Inu mukukhulupirira kuti iko kuchila? 158 Dona pafupi ndi inupo ali ndi kutaya kwa magazi nayenso, ndipo iye ali ndi vuto la nsana. Inu mukukhulupirira kuti Mulungu akuchiritsani inu? Inu mukutero? Kwezani dzanja lanu ndi kulandira izo. Khulupirirani. 159 Dona uyu pafupi ndi inu ali ndi vuto ndi miyendo yake ndi ntchafu zake. Kodi inu mukukhulupirira kuti uko nkulondola, dona? Inu mukukhulupirira kuti inu muchiritsidwa? Chabwino, kwezani mmwamba dzanja lanu, nkuti, “Ine ndikulandira izo.” 160 Chabwino, dona pafupi ndi iye ali ndi matenda. Inu mukukhulupirira kuti Mulungu achiza matendawo, dona wamng’ono amene mwavala magalasi? Kwezani mmwamba dzanja lanu, nkuti, “Ine ndikuwalandira iwo.” Chabwino, khulupirirani izo. 161 Dona pafupi ndi iye ali ndi vuto la impso. Kodi inu mukukhulupirira kuti Mulungu achiza vuto la impsolo, dona? Chabwino, kwezani mmwamba dzanja lanu, landirani iwo. 162 Msungwana wamng’ono pafupi ndi iye ali ndi chapakhosi. Inu mukukhulupirira kuti Mulungu achiza chotupacho apo? Kwezani mmwamba dzanja lanu, alandireni iwo. 163 Ndi angati mukukhulupirira ndi mtima wanu wonse? Ndiye imani pa mapazi anu ndi kuwalandira iwo. Imirirani mu Kukhalapo kwa Mulungu wa Abrahamu, Isaki, ndi wa Yakobo. 164 Mu Dzina la Ambuye Yesu Khristu siyani Mzimu Woyera ugwere mu nyumba muno tsopano ndi kumuchiritsa munthu aliyense mu Kukhalapo Kwaumulungu! `

MULUNGU NDI WODZITANTHAUZIRA YEKHA

27

Mulungu Ndi Wodzitanthauzira Yekha, Vol. 13 No. 4 (God Is His Own Interpreter, Vol. 8 No. 6) Uthenga uwu wa M’bale William Marrion Branham wolalikidwa mu Chingelezi pa Lachitatu usiku, Feburuwale 5, 1964, ku Kern County Fairgrounds mu Bakersfield, California, U.S.A., unatengedwa kuchokera pa matepi ojambulidwa ndi maginito nudindidwa mosachotsera mawu ena mu Chingelezi. Kumasulira uku kwa Chichewa kunadindidwa mchaka cha 2000 ndi Voice of God Recordings.

VOICE OF GOD RECORDINGS P.O. Box 950, Jeffersonville, Indiana 47131 U.S.A.

J ust O ne M ore T ime , L ord

1

Copyright notice All rights reserved. This book may be printed on a home printer for personal use or to be given out, free of charge, as a tool to spread the Gospel of Jesus Christ. This book cannot be sold, reproduced on a large scale, posted on any website other than www.branham.org, stored in a retrieval system, translated into other languages, or used for soliciting funds without the express written permission of Voice Of God Recordings®. For more information or for other available material, please contact:

Voice Of God Recordings

P.O. Box 950, Jeffersonville, Indiana 47131 U.S.A. www.branham.org